Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 180
  • Kodi Chiyembekezo Ndingachipeze Kuti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chiyembekezo Ndingachipeze Kuti?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kukhala ndi chiyembekezo?
  • Kodi Baibulo limathandiza anthu kuti aziyembekezera zotani?
  • Pitirizani Kulimbitsa Chiyembekezo Chanu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Yambani Chaka cha 2023 Muli Ndi Chiyembekezo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nkhani Zina
  • Yembekezani Yehova Kuti Mukhale Olimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Chiyembekezo Chodalirika Mungachipeze Kuti?
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 180
Mzimayi akuyang’anitsitsa kutsogolo ndi chiyembekezo.

Kodi Chiyembekezo Ndingachipeze Kuti?

Yankho la m’Baibulo

Baibulo limanena kuti Mulungu akufuna kutipatsa “chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino.”a (Yeremiya 29:11) Ndipotu chimodzi mwa zifukwa zimene Mulungu anatipatsira Malemba, ndi choti ‘tikhale ndi chiyembekezo komanso kuti atithandize kupirira ndiponso kutilimbikitsa.’ (Aroma 15:4) Monga mmene tionere, malangizo anzeru a m’Baibulo angatithandize kuthana ndi mavuto amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku. Komanso zimene Baibulo limalonjeza zingatithandize kuti tiziyembekezera kuti zinthu zidzakhala bwino mtsogolo.

Zimene zili munkhaniyi

  • Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kukhala ndi chiyembekezo?

  • Kodi Baibulo limathandiza anthu kuti aziyembekezera zotani?

  • Mavesi a m’Baibulo onena za chiyembekezo

Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kukhala ndi chiyembekezo?

Baibulo limatithandiza kukhala ndi chiyembekezo, potisonyeza zimene tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

  • Muzidalira malangizo anzeru opezeka m’Baibulo. Lemba la Salimo 119:105 limati: “Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga, ndi kuwala kounikira njira yanga.” Kuwala kwa mphamvu kungatithandize m’njira ziwiri. Choyamba, kungatithandize kuunikira zinthu zimene zili patsogolo pathu. Ndipo chachiwiri, kungatithandize kuunikira zinthu zomwe zili patali. Mofanana ndi zimenezi, mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuthana ndi mavuto amene tikukumana nawo panopa ndipo zimenezi zingathandize kuti tsiku lililonse tizikhala ndi chiyembekezo. Zimene Baibulo limaphunzitsa zingatithandize kuti tikhalenso ndi mphamvu komanso zingatithandize kukhala wosangalala. (Salimo 19:7, 8) Ndiponso Baibulo limatithandiza kudziwa zimene Mulungu akufuna kudzachitira anthu komanso dziko lapansi mtsogolo. Kuyembekezera zinthu zimenezi kungatithandize kuti tizikhala osangalala.

  • Muzilola kuti ena akuthandizeni: Nthawi zina tikathedwa nzeru chifukwa cha mavuto, tingayambe kumadzipatula, osamafuna kucheza ndi achibale ndiponso anzathu. Koma Baibulo limanena kuti kuchita zimenezi ndi kosathandiza chifukwa kungachititse kuti tisankhe zinthu molakwika komanso mosaganiza bwino. (Miyambo 18:1) Achibale komanso anzathu angatithandize kuti tiziganiza bwino. Akhozanso kutithandiza kupeza njira zabwino zothanirana ndi vuto limene takumana nalo. (Miyambo 11:14) Komanso akhoza kutitonthoza komanso kutilimbikitsa ndipo zimenezi zingatipatse mphamvu zoti tipirire mpaka zinthu zitayambiranso kuyenda bwino.—Miyambo 12:25.

  • Muzipemphera kwa Mulungu. Baibulo limati: “Umutulire Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakuchirikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.” b (Salimo 55:22) Ndi pomveka kuti Baibulo limanena kuti Yehova ndi “Mulungu amene amapereka chiyembekezo.” (Aroma 15:13) Mukhoza kumuuza “nkhawa zanu zonse” muli ndi chikhulupiriro kuti akumverani, chifukwa amakuderani nkhawa. (1 Petulo 5:7) Ndipotu Baibulo limati Mulungu, “adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu.”—1 Petulo 5:10.

  • Muzilola kuti mayesero azikuthandizani kukhulupirira kwambiri zimene Mulungu walonjeza. Baibulo limalonjeza kuti munthu womvera Mulungu “adzakhala mwabata ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.” (Miyambo 1:33) Nthawi ina ku Australia kutachitika mphepo yamkuntho, katundu wa mayi wina dzina lake Margaret, anawonongeka. Koma mayiyu sankangokhalira kudandaula chifukwa anazindikira kuti chuma sichikhalitsa. Kungoyambira nthawi imeneyo, anayamba kuganizira za zinthu zofunika kwambiri zomwe ndi banja lake, anzake, ubwenzi wake ndi Mulungu komanso chiyembekezo chimene chimapezeka m’Baibulo.— Salimo 37:34; Yakobo 4:8.

Kodi Baibulo limathandiza anthu kuti aziyembekezera zotani?

Baibulo limalonjeza kuti posachedwa, anthu onse adzakhala ndi tsogolo labwino komanso kuti dzikoli lidzakhala malo abwino kwambiri. Mavuto amene tikukumana nawo masiku ano ndi umboni woti tili ‘m’masiku otsiriza’ a dzikoli. (2 Timoteyo 3:1-5) Posachedwapa, Mulungu adzakonza zinthu padzikoli ndipo adzathetsa zinthu zopanda chilungamo komanso mavuto onse. Iye adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito boma lomwe limatchedwa kuti Ufumu wa Mulungu. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 11:15) Yesu ankaganizira za boma limeneli pomwe ananena mu pemphero lachitsanzo kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike . . . pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

Baibulo limanena momveka bwino zimene Mulungu akufuna kudzachitira anthu. Onani mavuto ena amene Ufumu wa Mulungu udzathetse:

  • Sikudzakhalanso njala. “Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.”—Salimo 67:6.

  • Sikudzakhalanso matenda. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.

  • Sikudzakhalanso imfa. Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso [mwa anthu onse], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

a Timayembekezera chinthu chimene tikuchilakalaka komanso chomwe tikukhulupirira kuti tichipeza. Chiyembekezo chikhoza kukhala chinthu chimene tikuchiyembekezera kapena chimene chikutipangitsa kuyembekezera zinazake.

b Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.—Salimo 83:18.

Mavesi a m’Baibulo onena za chiyembekezo

Yobu 5:16: “Wonyozeka amapeza chiyembekezo.”

Tanthauzo lake: Anthu amene amaona kuti amasalidwa masiku ano, ayenera kukhulupirira kuti Mulungu adzawasamalira ngati atamupempha kuti awathandize.

Salimo 27:14: “Yembekezera Yehova. Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Yembekezera Yehova.”

Tanthauzo lake: Tikamakhulupirira Yehova Mulungu timapeza mphamvu komanso timalimba mtima. Yehova sadzasiya anthu amene amamukhulupirira.

Salimo 62:5: “Yembekezera Mulungu modekha, iwe moyo wanga, chifukwa chiyembekezo changa chichokera kwa iye.”

Tanthauzo lake: Anthu amene amadalira Mulungu akamakumana ndi mavuto sakayikira kuti adzawathandiza panthawi yake.

Miyambo 20:22: “Usanene kuti: ‘Ndidzabwezera choipa.’ Khulupirira Yehova ndipo iye adzakupulumutsa.”

Tanthauzo lake: Munthu wina akatikhumudwitsa tikhoza kupewa kumubwezera ngati timakhulupirira Yehova. Iye ali ndi mphamvu komanso amafunitsitsa kutiteteza komanso kuthetsa mavuto amene tikukumana nawo.

Aheberi 6:19: “Chiyembekezo [Chachikhristu] chimene tili nachochi chili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika.”

Tanthauzo lake: Mofanana ndi nangula amene amathandiza sitima kuti isatengeke ndi mphepo, chiyembekezo chotsimikizirika cha madalitso amene Mulungu watilonjeza chingatithandize kuchepetsa nkhawa. Komanso chingatithandize kukhala olimba kuti tipirire mavuto.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena