Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwfq nkhani 11
  • Kodi a Mboni za Yehova Ndi Gulu Lampatuko la ku America?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi a Mboni za Yehova Ndi Gulu Lampatuko la ku America?
  • Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Nkhani Yofanana
  • Akristu ndi Chitaganya cha Anthu Lerolino
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Mboni za Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Mafunso Amene Anthu Amakonda Kufunsa
    Galamukani!—2010
  • Kodi Mboni za Yehova Ndikagulu Kotsatira Munthu?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
ijwfq nkhani 11
Gulu la anthu osangalala ochokera m’mayiko osiyanasiyana

Kodi a Mboni za Yehova Ndi Gulu Lampatuko la ku America?

Likulu lathu limene limayang’anira ntchito ya padziko lonse lili ku United States of America. Koma si ndife gulu lampatuko la ku America pa zifukwa zotsatirazi:

  • Anthu ena amati gulu lampatuko limachita kuchoka m’chipembedzo china chachikulu kapena chodziwika bwino. Koma a Mboni za Yehova sanachite kuchoka m’chipembedzo china. M’malomwake, timaona kuti tinakhazikitsanso Chikhristu chimene chinalipo m’nthawi ya atumwi.

  • A Mboni za Yehova akugwira ntchito yawo yolalikira mwakhama m’mayiko oposa 230. M’dziko lililonse limene tikukhala, timaonetsetsa kuti choyamba, tikumvera ndiponso kugonjera Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu, osati boma la ku America kapena boma lina lililonse la anthu.—Yohane 15:19; 17:15, 16.

  • Mfundo zonse zimene timaphunzitsa zimachokera m’Baibulo, osati kwa mtsogoleri wina wachipembedzo wa ku United States.—1 Atesalonika 2:13.

  • Ife timatsatira Yesu Khristu, osati mtsogoleri winawake.—Mateyu 23:8-10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena