Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 32
  • Kodi Kukhala ndi Ulemu N’kofunikadi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kukhala ndi Ulemu N’kofunikadi?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene muyenera kudziwa zokhudza kukhala ndi ulemu
  • Zimene mungachite kuti musinthe
  • Kulimirira Mayendedwe Achikristu M’dziko Lopanda Mayendedwe
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Mayendedwe Anu Ayenere Uthenga Wabwino”
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Khalidwe Labwino Lili Chizindikiro Chapadera cha Anthu a Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Tiyenera Kukhala Aulemu Popeza Ndife Atumiki a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 32
Mnyamata wanyamula katundu wa mayi wachikulire

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Kukhala ndi Ulemu N’kofunikadi?

‘Palibe amene amanditsegulira chitseko, ndiye palibe chifukwa choti ineyo ndizitsegulira chitseko anthu ena.’

‘Pali zinthu zofunika kwambiri zoti ndiziganizira, osati mawu osafunika kwenikweni ngati akuti “chonde,” “zikomo” kapena “pepani.”’

‘Palibe chifukwa chosonyezera ulemu kwa abale anga. Ndife a pachibale basi.’

Kodi inuyo mukugwirizana ndi mfundo, ngakhale imodzi, pa mfundo zimene zili pamwambazi? Ngati zili choncho, ndiye kuti mwina simukudziwa zonse zokhudza kufunika kokhala ndi ulemu.

  • Zimene muyenera kudziwa zokhudza kukhala ndi ulemu

  • Zimene mungachite kuti musinthe

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Zimene muyenera kudziwa zokhudza kukhala ndi ulemu

Kukhala ndi ulemu kungakuthandizeni pa mbali zitatu zotsatirazi:

  1. Mbiri yanu. Anthu angakuoneni kuti ndinu munthu wabwino kapena ayi, potengera zimene mumachitira anthu ena. Ngati muli ndi ulemu, anthu angakuoneni kuti ndinu wokhwima nzeru, ndipo angamakusonyezeni ulemu. Koma ngati muli wamwano, anthu angaone kuti mumangoganizira zanu zokha. Zimenezi zingachititse kuti muvutike kupeza ntchito ndiponso musapeze mwayi wochita zinthu zina zimene zingakuthandizeni. Baibulo limati: “Munthu wankhanza amachititsa kuti thupi lake linyanyalidwe.”—Miyambo 11:17.

  2. Ubwenzi wanu ndi ena. Baibulo limati: “Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akolose 3:14) Zimenezi ndi zoona, makamaka pa nkhani yokhudza ubwenzi ndi anthu ena. Anthu amakonda kucheza ndi munthu waulemu komanso wakhalidwe labwino. Koma palibe amene angafune kumacheza ndi munthu wamwano komanso wakhalidwe loipa.

  3. Mmene anthu angamachitire nanu zinthu. Mtsikana wina dzina lake Jennifer anati: “Nthawi zonse ukamachita zinthu mwaulemu, m’kupita kwa nthawi, ngakhale anthu amwano kwambiri akhoza kusintha n’kuyamba kukulemekeza.” Koma zimenezi sizingachitike ngati inunso mumachita zinthu mopanda ulemu. Baibulo limati: “Muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”—Mateyu 7:2.

Mfundo yofunika kwambiri: Tsiku ndi tsiku timafunika kulankhula kapena kuchita zinthu ndi anthu ena. Mmene mumachitira zinthu pa mbali imeneyi zingachititse kuti anthu azikulemekezani kapena ayi. Choncho kunena mwatchutchutchu, kukhala ndi ulemu n’kofunika kwambiri.

Zimene mungachite kuti musinthe

  1. Dzifufuzeni kuti mudziwe ngati mumasonyeza ulemu kwa ena. Dzifunseni mafunso ngati awa: ‘Kodi anthu akuluakulu ndimalankhula nawo mwaulemu? Kodi ndimalankhula kawirikawiri mawu ngati “chonde,” “zikomo” komanso “pepani”? Ndikamalankhula ndi ena, kodi ndimachitanso zinthu zina, monga muwerenga kapena kulemba mameseji? Kodi ndimasonyeza ulemu kwa makolo ndiponso abale anga, kapena ndimaona kuti ndi osafunika kuwasonyeza ulemu chifukwa ndi “abale anga”?’

    Baibulo limati: “Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.”—Aroma 12:10.

  2. Zimene mukufuna kuchita. Lembani zinthu zitatu zimene mukuona kuti mukufunikira kusintha. Mwachitsanzo, mtsikana wina wazaka 15, dzina lake Allison, anati: “Ndikufunika kumamvetsera kwambiri m’malo molankhula kwambiri.” David, wazaka 19, ananena kuti akufunika kupewa kuwerenga ndi kulemba mameseji akakhala ndi achibale ake kapena anzake. Iye anati: “Kuchita zimenezi n’kupanda ulemu. Zimakhala ngati ukuuza anthu amene uli nawowo kuti, sindikufuna kucheza ndi inuyo. Kuli bwino ndizicheza ndi amene ndikulemberana naye mamesejiwa.” Nayenso Edward, mnyamata wazaka 17, ananena kuti akufunika kusiya kudula mawu anthu ena akamalankhula. Ndipo Jennifer amene tamutchula poyamba uja ananena kuti akufunika kuyesetsa kumasonyeza ulemu kwa anthu akuluakulu. Iye anati: “Poyamba, ndinkangopereka moni mwachidule kenako n’kupitiriza kucheza ndi achinyamata anzanga. Koma panopa ndikuyesetsa kucheza ndi anthu achikulire kuti ndiwadziwe bwino. Zimenezi zandithandiza kwambiri kuti ndizichita zinthu mwaulemu.”

    Baibulo limati: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.

  3. Muziona ngati pali kusintha. Kwa mwezi wathunthu, muziona ngati mukusintha pa nkhani ya malankhulidwe ndi zochita zanu. Mweziwo ukatha, dzifunseni kuti: ‘Kodi kukhala ndi ulemu kwathandiza kuti ndikhale munthu wabwinopo? Nanga ndi zinthu ziti zimene ndikufunikirabe kusintha?’ Mukatero, onani zimene mungachite kuti musinthe.

    Baibulo limati: “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.”—Luka 6:31.

Kodi mukudziwa? Zinthu zimene mungachite posonyeza ulemu kudera lina, zingaoneke ngati mwano ngati mutachita zomwezo kudera linanso. Mwachitsanzo, ku Japan anthu amavula nsapato asanalowe m’nyumba posonyeza ulemu. Koma pali mayiko ena amene angati munthu atavula nsapato asanalowe m’nyumba, anthu akhoza kumuona kuti ndi wopanda khalidwe. Kodi kwanuko, anthu amayembekezera kuti munthu waulemu azichita zotani?

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

Selena

Selena

“Ukamachita zinthu mwaulemu, anthu amaona. Nthawi zambiri, ulemu ndi khalidwe loyamba limene ena amaona komanso kuyamikira. Iwenso umasangalala ukamachita zinthu mwaulemu chifukwa umadziwa kuti ukuchita zinthu zabwino.”

Megan

Megan

“Ukamachita zinthu mopanda ulemu, anthu amaona kuti ndiwe wachibwana. Koma ukamachita zinthu mwaulemu ndiponso moganizira ena, anthu amakulemekeza.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena