Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwbq nkhani 128
  • Kodi Mawu Oti Puligatoliyo Amapezeka M’Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mawu Oti Puligatoliyo Amapezeka M’Baibulo?
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Baibulo limanena
  • Kodi Akufa Amafuna Chithandizo Chanu?
    Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Purigatoriyo
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Zowonadi Ponena za Helo
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Mungalikhulupirire Baibulo?
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
ijwbq nkhani 128
Chithunzi chomwe munthu wina anajambula chosonyeza ku puligatoliyo

Kodi Mawu Akuti Puligatoliyo Amapezeka M’Baibulo?

Zimene Baibulo limanena

Ayi. M’Baibulo simupezeka mawu akuti “puligatoliyo,” ndipo siliphunzitsa kuti mizimu ya anthu amene amwalira imakayeretsedwa ku puligatoliyo.a Taonani zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza uchimo ndi imfa zomwe ndi zotsutsana ndi chiphunzitso cha puligatoliyo.

  • Kukhulupirira magazi a Yesu ndi kumene kumayeretsa munthu ku uchimo, osati kupita ku puligatoliyo. Baibulo limanena kuti “magazi a Yesu Mwana [wa Mulungu] akutiyeretsa ku uchimo wonse” komanso limati “Yesu Khristu . . . anatimasula ku machimo athu ndi magazi ake.” (1 Yohane 1:7; Chivumbulutso 1:5) Yesu anapereka “moyo wake dipo la anthu ambiri” kuti awawombole ku uchimo.—Mateyu 20:28, Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu.

  • Anthu amene amwalira sadziwa chilichonse. “Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Munthu amene wamwalira sangamve china chilichonse, choncho sizingatheke kuti ayeretsedwe ndi moto wa ku puligatoliyo.

  • Munthu samalangidwa chifukwa cha machimo pambuyo poti wamwalira. Baibulo limanena kuti “malipiro a uchimo ndi imfa” komanso limati “munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” (Aroma 6:7, 23) Choncho, imfa ndi chilango chokwanira cha uchimo.

Kodi chiphunzitso cha puligatoliyo n’chiyani?

Malinga ndi zimene tchalitchi cha Katolika chimaphunzitsa, puligatoliyo amatanthauza malo amene mizimu ya anthu omwe amwalira imakalapa chifukwa cha machimo amene sanakhululukidwe komanso kuyeretsedwa.b Malinga ndi zimene Katekisimu wa Katolika amanena, kuyeretsedwa kumeneku ndi kofunika n’cholinga choti munthu akhale “woyenera kulowa m’chikondwerero chosatha” kumwamba. Katekisimuyu amanenanso kuti “chikhalidwe cha Tchalitchi . . . chimanena za moto woyeretsa,” monga mmene chithunzi chomwe chili mu nkhani ino chikusonyezera. Komabe, zimenezi si zimene Baibulo limaphunzitsa.

Kodi chiphunzitso cha puligatoliyo chinachokera kuti?

Anthu a ku Giriki kale ankakhulupirira Limbo komanso puligatoliyo. Chifukwa cha nzeru za Agiriki, Clement wa mumzinda wa Alexandria, ananena motsimikiza kuti akufa akhoza kuyeretsedwa ku machimo awo ndi moto. Komabe, mogwirizana ndi buku lakuti The History of Christian Doctrines, anali Papa Gregory Wamkulu amene anatsindika zoti chikhulupiriro cha moto wa puligatoliyo ndi chosakayikitsa. Buku limeneli limanenanso kuti Gregory, yemwe anali papa kuyambira mu 590 mpaka 604 C.E, “nthawi zambiri amatchedwa monga “woyambitsa wa puligatoliyo.’” Tchalitchi cha Katolika chinafotokoza chiphunzitso chake cha puligatoliyo pamsonkhano wa ku Lyons mu 1274 komanso wa ku Florence mu 1439 ndipo tchalitchichi chinabwerezanso za chiphunzitsochi pamsonkhano wa ku Trent mu 1547.

a Ponena za puligatoliyo, buku lina linati, “m’Mauthenga Abwino mulibe mawu amenewa.” (Orpheus: A General History of Religions) Buku linanso limati: “Tinganene kuti chiphunzitso cha Chikatolika cha puligatoliyo ndi chochokera ku miyambo, osati Malemba Oyera.”—New Catholic Encyclopedia Buku Lachiwiri, Volume 11, tsamba 825.

b Onani buku lakuti New Catholic Encyclopedia, Second Edition, Volume 11, tsamba 824.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena