Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 83
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamagonje Poyesedwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamagonje Poyesedwa?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene muyenera kudziwa
  • Zimene mungachite
  • Mungatani Kuti Musamagonje Mukakumana ndi Mayesero?
    Galamukani!—2014
  • Kugonjetsa Kufooka Kwaumunthu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisagonje Poyesedwa?
    Galamukani!—2008
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamakopeke Ndi Zochita za Anzanga?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 83
Mnyamata waona anthu omwe ali pa chibwenzi ndipo nayenso wakopeka nazo, anyamata awiri akuyang’ana chipangizo chamakono ndipo mtsikana akuwadutsa

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamagonje Poyesedwa?

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili ndi ine.” (Aroma 7:21) Kodi inuyo munakhalapo ndi maganizo amenewa? Ngati zili choncho, nkhaniyi ingakuthandizeni kuti musamachite zinthu zoipa zimene mukulakalaka.

  • Zimene muyenera kudziwa

  • Zimene mungachite

  • Zimene anzanu anena

Zimene muyenera kudziwa

Nthawi zambiri munthu amafuna kuchita zoipa chifukwa chokakamizidwa ndi anzake. Paja Baibulo limanena kuti “kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto15:33) Anzanu komanso zosangalatsa zimene mumakonda zingakuchititseni kuti muyambe kulakalaka zinthu zoipa moti mukhoza ‘kutsatira khamu la anthu pochita zoipazo.’—Ekisodo 23:2.

“Mukamafunitsitsa kuti anthu ena azikukondani ndiponso kufuna kuti musakhale otsalira, mukhoza kuchita chilichonse chimene anthuwo akufuna.”—Jeremy.

Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani mungavutike kupewa zoipa ngati mumafunitsitsa kuti anthu ena azikukondani?—Miyambo 29:25.

Mfundo yofunika kwambiri: Musalole kuti anzanu akukakamizeni kuchita zinthu zoipa.

Zimene mungachite

Muzidziwa mfundo zimene mumayendera. Ngati simukudziwa bwino zimene mumakhulupirira, mungakhale ngati chidole chimene chimangochita chilichonse chimene anthu ena akufuna. Choncho ndi bwino kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Tsimikizirani zinthu zonse. Gwirani mwamphamvu chimene chili chabwino.” (1 Atesalonika 5:21) Mukadziwa bwino mfundo zimene mumakhulupirira, simungavutike kuzitsatira ndiponso kupewa kuchita chilichonse chosemphana ndi mfundozo.

Zoti muganizire: N’chifukwa chiyani mumakhulupirira kuti mfundo za Mulungu ndi zothandiza?

“Ndaona kuti ndikamatsatira mfundo zimene ndimakhulupirira popanda kugonja ndikayesedwa, anthu ena amandilemekeza kwambiri.”—Kimberly.

Chitsanzo chabwino cha m’Baibulo: Danieli. Ali wachinyamata, Danieli “anatsimikiza mumtima mwake” kuti azitsatira malamulo a Mulungu.—Danieli 1:8.

Mnyamata wamangidwa manja ndi miyendo ndipo anthu akumuyendetsa ngati chidole

Ngati simukudziwa bwino zimene mumakhulupirira, mungayambe kukhala ngati chidole chimene chimangochita chilichonse chimene anthu ena akufuna

Muzidziwa mavuto anu. Baibulo limanena kuti pali “zilakolako zaunyamata,” kapena kuti zinthu zimene achinyamata amalakalaka kwambiri. (2 Timoteyo 2:22) Zinthuzi zingakhale monga kulakalaka kugonana, kufuna kuti musakhale otsalira komanso kufuna ufulu wosagwirizana ndi msinkhu wanu.

Zoti muganizire: Baibulo limanena kuti “munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake.” (Yakobo 1:14) Kodi ndi zinthu zoipa ziti zomwe inuyo mumalakalaka kwambiri?

“Muyenera kudzifufuza moona mtima kuti mudziwe mayesero amene angakugonjetseni mosavuta. Muyenera kufufuza mfundo zimene zingakuthandizeni kuti muzipewa kuchita zoipazo ndiponso kulemba mfundo zimene mungatsatire. Izi zingakuthandizeni kuti musadzagonje mukadzayesedwa.”—Sylvia.

Chitsanzo chabwino cha m’Baibulo: Davide. Nthawi zina ankalolera kuchita zinthu zimene anzake ankafuna komanso zimene iye ankalakalaka. Koma Davide ankaphunzirapo kanthu pa zimene ankalakwitsa ndipo ankayesetsa kusintha. Paja iye anapempha Yehova kuti: “Lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.”—Sal. 51:10.

Musalole kugonja. Baibulo limati: “Musalole kuti choipa chikugonjetseni.” (Aroma 12:21) Izi zikutanthauza kuti mukhoza kusankha kuchita zinthu zabwino ngakhale mutayesedwa.

Zoti muganizire: Kodi mungachite chiyani kuti musamagonje mukamayesedwa?

“Ndimaganizira zimene zingachitike ngati nditagonja poyesedwa. Kodi ndikhala wosangalala? Mwina koma kwa nthawi yochepa chabe. Koma kodi ndipitiriza kukhala wosangalala? Ayi, ndidzanong’oneza bondo. Ndiye kodi ndi bwino kuchita zoipazi? Ayi.”​—Sophia.

Chitsanzo chabwino cha m’Baibulo: Paulo. Ngakhale kuti Paulo ananena kuti ankalakalaka kuchita zoipa, ankadziletsa. Iye analemba kuti: “Ndikumenya thupi langa ndi kulitsogolera ngati kapolo.”—1 Akorinto 9:27.

Mfundo yofunika kwambiri: Inuyo ndi amene muli ndi udindo wosankha zimene mungachite mukayesedwa.

Musaiwale kuti zinthu zimene zingayese munthu sizikhalitsa. Mwachitsanzo, mlongo wina wazaka 20 dzina lake Melissa anati: “Zinthu zambiri zimene ndinkayesedwa nazo ndili kusekondale, sindimaziganizira n’komwe panopa. Zimenezi zimanditsimikizira kuti zinthu zimene ndikuyesedwa nazo panopa zidzathanso ndipo m’tsogolo ndidzaona kuti ndinachita bwino kwambiri kudziletsa.”

Zimene anzanu anena

Olivia

“Ndimatsimikizira mumtima zimene ndimafuna kuchita ndiponso kulimba mtima kuti ndizizitsatira. Zimenezi zimandithandiza kuti ndisagonje poyesedwa. Mwachitsanzo, ndikasankha zimene sindikufuna kuchita sindilola kuti ndisinthe kapena kutengeka ndi zimene anthu ena akuchita.”—Olivia.

Jared

“Achinyamata ambiri amafuna kutengera anzawo n’kumapita kumapate, kumwa mowa, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza ubongo komanso kugonana. Ndimaona kuti kukambirana ndi makolo anga kumandithandiza kuti ndizipewa kuchita zinthu zimenezi. Kukhala ndi zochita zambiri kumandithandizanso kuti ndizipewa kuchita zoipa.”—Jared.

Mayan

“Ndimavutika kwambiri kupewa kuchita zinthu zimene anthu ena angaone kuti ndi zabwinobwino koma ineyo ndimaona kuti sizingandithandize. Zimenezi zimachitika kwambiri posankha zosangalatsa. Muyenera kudziwa bwino mfundo zimene mumayendera kuti musamangotengera zimene anthu ena akuchita. Koma zimatenga nthawi kuti munthu afike podziwa bwino mfundozo.”—Mayan.

Julian

“Muyenera kudzifufuza moona mtima pa nkhani ya zimene mungayesedwe nazo. Muyenera kudziwa malo a pa intaneti amene angakhale ndi zinthu zomwe mungayesedwe nazo komanso zimene mudzachite zikaoneka. Muyenera kudziwiratu zimene mudzachite n’cholinga choti musadzagonje.”​—Julian.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena