KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?
Sitinaiwale Abale ndi Alongo Athu Powathandiza Pangozi Zogwa Mwadzidzidzi mu 2021
1 JANUARY, 2022
M’chaka cha utumiki cha 2021,a anthu padziko lonse ankakumanabe ndi mavuto obwera chifukwa cha mliri wa COVID-19. Monga mmene tinafotokozera m’nkhani yakuti “Kupereka Chithandizo Padziko Lonse pa Nthawi ya Mliri,” pofika pano tagwiritsa ntchito ndalama zokwana madolab mamiliyoni ambiri zothandiza pa mliriwu ndipo tinakhazikitsa Makomiti Othandiza pa Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi oposa 950.
Pamene anthu ankakumana ndi mavuto ambiri chifukwa cha mliriwu, panalinso ngozi zina zam’chilengedwe komanso zoyambitsidwa ndi anthu zimene zinakhudzanso abale ndi alongo athu padziko lonse. Pofuna kuthandiza pa ngozi zoposa 200 zomwe zinachitika, Komiti ya Ogwirizanitsa ya Bungwe Lolamulira, inavomereza kuti ndalama zokwana madola 8 miliyoni zigwiritsidwe ntchito, kuwonjezera pa ndalama zomwe zinaperekedwa pothandizira pa mliri wa COVID-19. Taonani mmene zopereka zanu zinagwirira ntchito pothandiza abale ndi alongo omwe anakhudzidwa ndi ngozi ziwiri zaposachedwapa.
Kuphulika kwa Phiri la Nyiragongo
Pa 22 May 2021, Phiri la Nyiragongo linayamba kuphulika ku Democratic Republic of the Congo. Chiphala chochokera m’phirili chinawononga nyumba, masukulu ndiponso madamu osungira madzi. Koma panalinso mavuto ena kuwonjezera pa mavuto amenewa. Kwa masiku angapo phirili litaphulika, mumzinda wa Goma munkagwa fumbi la poizoni komanso kunkachitika zivomerezi zambirimbiri. Anthu opitirira hafu ya mumzindawo anauzidwa kuti asamuke kaye. Anthu masauzande ambirimbiri anathawa ndipo ena anapita ku Rwanda.
Abale am’komiti yopereka chithandizo m’derali akupereka phala pa Nyumba ya Ufumu
Pa anthu amene anasamukawa panali a Mboni za Yehova pafupifupi 5,000. Ena mwa iwo nyumba zawo zinawonongeka pomwe zina zinathyoledwa ndi akuba eniake atathawa. Makomiti Othandiza pa Ngozi Zadzidzidzi m’dziko la Rwanda ndiponso m’dziko la Democratic Republic of the Congo anagwirira limodzi ntchito yopereka chithandizo. Pofotokoza zomwe komiti ina inachita, ofesi ya nthambi ya Congo (Kinshasa) inanena kuti: “Ngakhale kuti mumzindawo munali chipwirikiti komanso anali asanalengeze kuti anthu athawe, komiti yopereka chithandizo inali itayamba kale kugawa chakudya, madzi, zofunda ndiponso zovala.” M’tawuni ina yomwe abale athu oposa 2,000 anathawiramo, akomiti anamanga matenti, kupereka mamasiki ndiponso kufotokoza zomwe abalewo angachite kuti apewe kutenga matenda a COVID-19 komanso kolera.
Matumba a chakudya akuyezedwa asanatumizidwe kwa a Mboni amene akhudzidwa ndi ngozi
Pofika mwezi wachitatu kuchokera pamene ngoziyi inachitika, abale anali atagawa matani 6 a mpunga, matani 6 a ufa, matani atatu a mafuta ophikira ndiponso matani atatu a madzi. Pofuna kupewa kuwononga ndalama zambiri, ofesi ya nthambi inakonza zoti zakudya zochuluka zigulidwe m’dzikolo m’malo moitanitsa zakudya zodula kumayiko ena.
Mlongo wina yemwe nyumba yake yongomangidwa kumene inawonongeka ndi ngoziyi, anati: “Zinatiwawa ndipo tinakhumudwa kwambiri.” Koma kenako banja lake linalandira chithandizo ndiponso linalimbikitsidwa ndi mfundo za m’Malemba. Panopa mlongoyu akunena kuti: “Yehova watithandiza kupeza zomwe tikufunikira. Taona kuti Yehova amatinyamulira mavuto athu komanso amatithandiza kupirira.”
Mavuto Azachuma ku Venezuela
Anthu akhala akukumana ndi mavuto azachuma kwa zaka zambiri ku Venezuela. Abale athu m’dzikoli akupirira mavuto monga kusowa pokhala, kusowa chakudya ndiponso kuchuluka kwa zauchigawenga. Koma gulu la Yehova silinawaiwale.
Akulongedza matumba a mpunga kuti akawapereke m’madera osiyanasiyana ku Venezuela
M’chaka chautumiki chapitachi, gulu lathu linagwiritsa ntchito ndalama zopitirira madola 1.5 miliyoni pogula ndi kutumiza zakudya komanso sopo ku mabanja omwe analibiretu mtengo wogwira. Ofesi ya nthambi ya ku Venezuela inati: “Sizinali zophweka kutumiza matani a zakudya okwana 130 m’zigawo zonse za dzikolo mwezi uliwonse komanso kuonetsetsa kuti abale onse alandira chakudya.” Pofuna kuonetsetsa kuti chakudyachi chisaole, abalewa ankatumiza chakudya chosawonongeka msanga. Ofesi ya nthambi inanenanso kuti: “Tikumagula zakudya zambiri, zomwe zikupezeka kwambiri ndiponso zomwe zikutchipa pa nthawiyo. Kenako timazitumiza pogwiritsa ntchito njira yotchipa kwambiri.”
Chifukwa cha kusowa kwa mafuta a galimoto komanso magalimoto, abale achinyamata akuyenda mtunda wa makilomita 18 kupita ndi kubwera panjinga zakapalasa kuti akapereke zakudya kumpingo wawo
Leonel wa mu Komiti Yothandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi ku Venezuela, amakonda kwambiri utumiki wakewu. Iye anati: “Ntchito yopereka chithandizo ndi yapadera kwambiri. Utumiki wapaderawu wandithandiza kulimbitsa chikhulupiriro changa kungochokera pamene mkazi wanga anamwalira atadwala COVID-19. Ndimasangalala kuchita utumikiwu mwakhama komanso kuti ndikuthandiza abale. Ndadzionera ndekha kuti Yehova amakwaniritsa lonjezo lake lakuti sadzasiya anthu ake.”
M’bale wina yemwe ankatumikira mukomiti yopereka chithandizo m’mbuyomu nayenso akulandira chithandizo panopa. Iye anati: “Panopa ndi nthawi yakuti nanenso ndilandire chithandizo. Abalewa sanangotipatsa chithandizo chakuthupi chokha. Iwo anathandizanso ine ndi mkazi wanga kukhalabe osatekeseka. Anatisonyeza chikondi, kutitonthoza komanso kutilimbikitsa.”
Nthawi zina sizivuta kudziwa kuti kuchitika ngozi zam’chilengedwe pamene nthawi zina zimangochitika mwadzidzidzi. Komabe, nthawi zambiri gulu la Yehova limakwanitsa kuchita zinthu mwachangu popeza ndi kupereka chithandizo kwa abale ndi alongo omwe akhudzidwa. Zimenezi zimatheka chifukwa cha zopereka zanu. Njira zina zokhudza mmene mungaperekere zafotokozedwa pa donate.jw.org. Tikukuthokozani kwambiri chifukwa chakuti mumapereka mowolowa manja.
a Chaka cha utumiki cha 2021 chinayamba pa 1 September 2020, ndipo chinatha pa 31 August 2021.
b Ndalama za madola zomwe zikutchulidwa m’nkhaniyi ndi za ku United States.