KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?
Kuteteza Anthu pa Nyumba za Ufumu Panthawi ya COVID-19
1 OCTOBER, 2022
“Bungwe Lolamulira lakonza zoti mipingo yonse iyambirenso kusonkhana pamasom’pamaso kuyambira pa 1 April pokhapokha ngati malamulo aboma akuletsa anthu kuti azisonkhana pamodzi.” Chilengezochi chinaikidwa pa jw.org kumayambiriro kwa March 2022, ndipo abale ndi alongo padziko lonse anasangalala kwambiri kumva chilengezochi. Komabe chilengezochi chinaperekedwa mliri wa COVID-19 usanathe.a Koma kodi pankafunikira kupeza komanso kusintha zinthu zotani kuti anthu odzasonkhana atetezeke ku mliriwu? Koma kodi tikanakwanitsadi kusonkhana pamasom’pamaso m’Nyumba za Ufumu patatha zaka ziwiri osazigwiritsidwa ntchito?
Kwa miyezi yambiri abale anali atayamba kale kukonzekera kuti tiyambirenso kusonkhana m’Nyumba za Ufumu.
Kupeza Zinthu Zofunikira Mogwirizana Ndi Deralo
Patangotha mwezi umodzi wokha titasiya kusonkhana pamasom’pamaso mu 2020, Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga Padziko Lonse (WDC) ku Warwick, New York, inayamba kufufuza mmene mliri wa COVID-19 ungakhudzire nkhani yogwiritsa ntchito Nyumba za Ufumu. Dipatimentiyi inafufuzanso zomwe abale angachite kuti anthu odzasonkhana akhale otetezeka.
Zomwe zinkafunika kuti anthu akhale otetezeka m’nyumbazi, zinkasiyanasiyana potengera madera. M’bale Matthew De Sanctis amene amagwira ntchito mudipatimentiyi ananena kuti: “M’madera ena zinali zovuta kwambiri kupeza zipangizo zosambira m’manja. Ngati pa Nyumba ya Ufumu palibe mpopi, abale ankafunika kukagula madzi kapena kukatunga kumtsinje wapafupi kapenanso pachitsime. M’mayiko ena, boma linasintha zinthu zina pankhani yokhudza zipangizo zoziziritsira m’nyumba komanso zikwangwani zonena zaukhondo.”
Kodi abale anatani ndi kusintha kwa zinthu kumeneku? M’bale De Sanctis ananena kuti “Tinapeza kuti kugwiritsa ntchito zinthu zosafuna ndalama zambiri kunali kothandiza.” Mwachitsanzo, ku Papua New Guinea anayamba kugwiritsa ntchito mabigili a malita 20 okhala ndi mipopi. Choncho abale ankatha kupezera mipingo ya kumudzi zipangizo zosambira m’manja za ndalama zokwana madola 40 okha a ku United States. Pomwe pa Nyumba za Ufumu za ku Africa, panagulidwa zipangizo zabwino kwambiri zosambira m’manja zoposa 6,000 kuchokera kukampani ina ya ku Asia.
Makolo ankapereka chitsanzo chabwino kwa ana awo pokhala aukhondo
M’mayiko ena anaika mafani n’cholinga choti m’Nyumba za Ufumu muzikhala mpweya wabwino wokwanira. Mipingo yambiri inagula ndodo zitalizitali za maikolofoni n’cholinga choti ofalitsa asamagwire maikolofoniyo akafuna kupereka ndemanga. Panakonzedwanso zoti malo omwe anthu amagwirapo kawirikawiri monga mahandulo a zitseko komanso mipopi azipakidwa mankhwala ophera tizilombo. M’mipingo ina, abale anaika ku zimbudzi mipopi yomwe imatseguka yokha munthu akangoyandikizitsa manja kumpopiwo. M’dziko la Chile kuti akwanitse kusintha zina ndi zina pa Nyumba ya Ufumu iliyonse, pankafunika ndalama zokwana madola 1,400 a ku United States.
Ofalitsa sankagwira maikolofoni
Poyesetsa kuteteza abale ndi alongo omwe abwera pa Nyumba za Ufumu, abalewa ankayesetsanso kugwiritsa ntchito mosamala kwambiri ndalama zomwe abale ndi alongo amapereka. Mwachitsanzo, m’mayiko ena omwe boma limatha kuchotsa msonkho pa katundu wina, abale anakwanitsa kugula zipangizo zosambira m’manja komanso ndodo za maikolofoni popanda kulipira msonkho. Maofesi a nthambi ena anagwirizana zogulira limodzi zipangizozi n’cholinga choti agule zipangizo zambiri kuti apulumutse ndalama. Maofesi a nthambi komanso Dipatimenti Yothandiza Kugula Zinthu Padziko Lonse anakonza zoti azigula zinthu mwachindunji kuchokera ku makampani amene amapanga zinthuzo, zimenezi zinathandiza kuti azigula zipangizozo motchipa komanso kuti zizifika mwamsanga.
Malo opakira sanitaiza m’manja
“Ndinayamba Kumva Kuti Ndine Wotetezeka Ngati Mmene Ndinkafunira”
Kukonza zoti pa Nyumba za Ufumu pakhale zipangizo zopewera COVID-19, kunathandiza anthu omwe abwera kudzasonkhana kumva kuti ndi otetezeka. Mlongo Dulcine wa ku Peru “anali ndi mantha” atamva kuti tiyambiranso kusonkhana ku Nyumba ya Ufumu. Iye ananena kuti: “Ndinapezekapo ndi COVID-19 mliriwu utangoyamba kumene ndiye ndinkachita mantha ndikaganizira zoyambiranso kupita ku Nyumba ya Ufumu chifukwa ndinkaona kuti ndikhoza kutenganso matendawa. Koma nditafika pa Nyumba ya Ufumu, ndinaona kuti abale anali ataika kale njira zosiyanasiyana zopewera mliriwu monga, kuika mankhwala a sanitaiza m’malo osiyanasiyana, kukhala ndi ndodo zitalizitali za maikolofoni komanso anakonza zoti Nyumba ya Ufumu izipoperedwa mankhwala misonkhano isanayambe komanso ikatha. Chifukwa cha zimenezi ndinayamba kumva kuti ndine wotetezeka ngati mmene ndinkafunira.”b
Kupaka mankhwala opha tizilombo m’Nyumba ya Ufumu
Mlongo Sara wa ku Zambia, anakumana ndi vuto losiyana ndi limeneli. Iye ananena kuti: “Miyezi ingapo yapitayo, mwamuna wanga anamwalira ndi COVID-19. Ndinkada nkhawa kuti ndidzamva bwanji kwa nthawi yoyamba ndikapita ku Nyumba ya Ufumu popanda iye.” Ndiye kodi panopa amamva bwanji akafika ku Nyumba ya Ufumu? Iye ananena kuti: “Kusonkhana pamasom’pamaso kwandithandiza kutsimikiza kuti Yehova ali nafe m’masiku otsiriza ano. Kuposa kale lonse, panopa ndimamva kuti ndimalimbikitsidwa, kukondedwa kwambiri komanso kupeza thandizo limene ndimafunikira kuchokera kwa akulu komanso abale ndi alongo onse.”
Kusangalala kuti ayambiranso kusonkhana pamasom’pamaso
Padziko lonse lapansi abale athu okondedwa akusangalala kwambiri chifukwa cha mwayi woyambiranso kusonkhana m’Nyumba za Ufumu. Tikuyamikira kwambiri chifukwa cha zopereka zanu, zomwe zambiri mwa ndalamazi zakhala zikuperekedwa kudzera pa donate.jw.org. Zoperekazi zimathandiza kuti tizikonza malo athu olambirira kuti anthu odzasonkhana azikhala malo abwino komanso otetezeka.
a Potengera mmene zinthu zinalili, ena anapitirizabe kuchita misonkhano kudzera pa vidiyokomfelensi kapena pafoni.
b Kuonjezera pamenepo, aliyense ankalimbikitsidwa kuvala masiki pamisonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu.