22 Pambuyo pake anasamuka kumeneko, ndipo anakumbanso chitsime china. Koma sanakanganirane chitsime chimenechi. Choncho iye anachipatsa dzina lakuti Rehoboti nʼkunena kuti: “Chifukwa chake nʼchakuti, tsopano Yehova watipatsa malo okwanira, ndipo watipangitsa kuti tichulukane mʼdziko lino.”+