22 Ngati amuna akumenyana ndipo avulaza kwambiri mkazi woyembekezera, moti mkaziyo nʼkubereka mwana nthawi yake isanakwane+ koma palibe amene wamwalira, wovulaza mkaziyo azimulipiritsa mogwirizana ndi zimene mwamuna wa mkaziyo angagamule. Azikapereka malipirowo kudzera kwa oweruza.+