15 Muzichita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda zofufumitsa masiku 7 pa nthawi imene inaikidwa mʼmwezi wa Abibu+ mogwirizana ndi zimene ndinakulamulani, chifukwa munatuluka mu Iguputo mʼmwezi umenewu. Ndipo palibe amene ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.+