31 Dziko limene ndidzakupatsani lidzayambira ku Nyanja Yofiira mpaka kunyanja ya Afilisiti, ndiponso kuyambira kuchipululu mpaka ku Mtsinje.+ Ndidzachita zimenezi chifukwa anthu okhala mʼdzikomo ndidzawapereka mʼmanja mwanu ndipo inu mudzawathamangitsa pamaso panu.+