-
Ekisodo 29:20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Uphe nkhosayo nʼkutengako magazi ake ndipo uwapake mʼmunsi pakhutu lakumanja la Aroni, ndi mʼmunsi pamakutu akumanja a ana a Aroni. Uwapakenso pazala zawo za manthu kudzanja lamanja ndi pazala zawo zazikulu za mwendo wakumanja, ndipo uwaze magaziwo mbali zonse za guwa lansembe.
-