5 Lamba woluka womangira efodi amene anamulumikiza ku efodiyo+ anali wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Anali wagolide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.