25 Ndiyeno wansembe azipha nkhosa yaingʼono yamphongo ya nsembe yakupalamula. Akatero azitenga ena mwa magazi a nsembe yakupalamulayo nʼkuwapaka mʼmunsi pakhutu lakumanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja.+