17 Muzibweretsa mitanda iwiri ya mkate wamʼnyumba mwanu kuti ikhale nsembe yoyendetsa uku ndi uku. Mitandayo izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Poiphika izikhala ndi zofufumitsa,+ ndipo muziipereka kwa Yehova monga zipatso zoyambirira kucha.+