20 Wansembe aziyendetsa uku ndi uku ana a nkhosa awiriwo pamodzi ndi mitanda ya mkate ya zipatso zoyambirira kucha, monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku yoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi zizikhala zinthu zopatulika kwa Yehova ndipo zizikhala za wansembe.+