38 Amene ankamanga msasa wawo kumʼmawa kwa chihema, kumbali yotulukira dzuwa, anali Mose ndi Aroni, ndiponso ana a Aroni. Ntchito yawo inali kutumikira mʼmalo opatulika, mʼmalo mwa Aisiraeli. Munthu wamba aliyense amene wayandikira malowo, ankayenera kuphedwa.+