21 Wansembeyo azilumbiritsa mkaziyo ndi lumbiro limene likuphatikizapo temberero. Iye aziuza mkaziyo kuti: “Yehova akuike kukhala chitsanzo cha temberero ndi lumbiroli pakati pa anthu a mtundu wako. Yehova achite zimenezo pofotetsa ntchafu yako ndi kutupitsa mimba yako.