11 Wansembeyo azitenga mwana mmodzi wa njiwa kapena wa nkhunda nʼkumupereka monga nsembe yamachimo. Azitenganso mwana wa njiwa kapena wa nkhunda winayo nʼkumupereka monga nsembe yopsereza kuti aphimbe machimo+ amene munthuyo anachita pokhudza munthu wakufa. Akatero aziyeretsa mutu wake pa tsikulo.