12 Kodi ndine ndinatenga pakati pa anthu onsewa? Ndine kodi ndinawabereka, kuti mundiuze kuti, ‘Uwanyamule pachifuwa chako mmene wantchito yolera mwana amanyamulira mwana woyamwa,’ pa ulendo wopita nawo kudziko limene munalumbira kuti mudzalipereka kwa makolo awo?+