25 Kenako Yehova anatsika mumtambo+ nʼkulankhula naye.+ Anatengako gawo lina la mzimu+ umene unali pa Mose nʼkuuika pa aliyense wa akulu 70 amenewo. Ndipo mzimuwo utangokhala pa iwo, anayamba kuchita zinthu ngati aneneri,+ koma anangochita zimenezi kamodzi kokhaka.