13 Munthu aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu, koma sanadziyeretse, wadetsa chihema cha Yehova.+ Munthu ameneyo aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa Isiraeli.+ Iye adakali wodetsedwa chifukwa sanawazidwe madzi oyeretsera.+ Choncho adzakhalabe wodetsedwa.