19 Munthu amene si wodetsedwa uja awaze munthu wodetsedwayo madziwo pa tsiku lachitatu komanso pa tsiku la 7.+ Ndipo pa tsiku la 7 lomwelo amuyeretse ku tchimo lake. Kenako amene akuyeretsedwayo achape zovala zake nʼkusamba ndi madzi, ndipo madzulo ake adzakhala woyera.