9 Koma pa tsiku la Sabata,+ muzipereka nsembe ana a nkhosa awiri amphongo opanda chilema. Muziwapereka pamodzi ndi ufa wosalala kuti ikhale nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta, ndipo uzikhala wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Muziperekanso nsembe yake yachakumwa.