2 Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa amphongo 7, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.