8 Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi. Nyama zonsezo zizikhala zopanda chilema.+