19 Mumange msasa kunja kwa msasawu, ndipo mukhalemo masiku 7. Aliyense amene wapha munthu komanso aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu wophedwa,+ adziyeretse+ pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku la 7. Mudziyeretse limodzinso ndi anthu amene mwawagwirawo.