47 Ndiyeno pa hafu imene anapereka kwa Aisiraeliwo, Mose anatengapo chamoyo chimodzi pa zamoyo 50 zilizonse, pa anthu ndi pa ziweto. Zinthu zimenezi anazipereka kwa Alevi+ amene ankatumikira pachihema cha Yehova,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.