15 Muzimupatsa malipiro ake tsiku lomwelo dzuwa lisanalowe,+ chifukwa iye ndi wosauka ndipo akudalira malipiro ake omwewo kuti akhale ndi moyo. Mukapanda kutero adzafuula kwa Yehova chifukwa cha zimene inuyo mwamuchitira ndipo mudzapezeka kuti mwachimwa.+