15 Yehova akadzapereka mpumulo kwa abale anu, ngati mmene waperekera kwa inu, nawonso abale anu akakatenga malo amene Yehova Mulungu akuwapatsa, mʼpamene inuyo mudzabwerere. Mudzabwerera kumalo anu amene Mose mtumiki wa Yehova wakugawirani, tsidya lino la Yorodano, kumʼmawa kuno.’”+