7 Muzidzawauza kuti: ‘Nʼchifukwa chakuti madzi amumtsinje wa Yorodano anagawikana chifukwa cha likasa+ la pangano la Yehova. Likasalo likudutsa mumtsinje wa Yorodano, madzi a mtsinjewo anagawikana. Miyalayi ndi yoti izikumbutsa Aisiraeli zimenezo mpaka kalekale.’”+