22 Ndiyeno asilikali amene analanda mzinda aja anatuluka mumzindamo kudzamenyana ndi amuna a ku Aiwo. Choncho amuna a ku Ai anali pakati pa Aisiraeli, ena mbali ino, ena mbali inayo. Aisiraeliwo anapha amuna a ku Ai, moti palibe amene anatsala kapena kuthawa.+