5 Choncho mafumu 5 a Aamoriwo,+ limodzi ndi magulu awo ankhondo, anasonkhana pamodzi ndipo anakamanga msasa pafupi ndi anthu a ku Gibiyoni nʼcholinga choti amenyane nawo. Mafumuwo anali mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Heburoni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi ndi mfumu ya ku Egiloni.