4 Iwo anapita kwa wansembe Eliezara,+ Yoswa mwana wa Nuni ndi atsogoleri, nʼkuwauza kuti: “Yehova ndi amene analamula Mose kuti atipatse cholowa pakati pa abale athu.”+ Choncho anawapatsa cholowa pakati pa azichimwene a bambo awo, pomvera lamulo la Yehova.+