29 Nʼzosatheka kuti ife lero tipandukire Yehova, nʼkusiya kutsatira Yehova+ pomanga guwa lansembe loti tiziperekerapo nsembe zopsereza, zambewu ndi nsembe zina, kusiya guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, limene lili patsogolo pa tenti yake yopatulika!”+