31 Koma Yowasi+ anauza onse amene anamuukirawo kuti: “Kodi inu mukuyenera kuteteza Baala? Kodi mukuyenera kumʼpulumutsa? Aliyense wofuna kumuteteza ayenera kuphedwa mʼmawa womwe uno.+ Ngati Baalayo ndi mulungu, adziteteze yekha+ chifukwa munthu wina wamugwetsera guwa lake lansembe.”