4 Kenako Yefita anasonkhanitsa amuna onse a ku Giliyadi+ nʼkumenyana ndi anthu a ku Efuraimu. Amuna a ku Giliyadi anagonjetsa anthu a ku Efuraimu, amene mʼmbuyomo ankati: “Ngakhale kuti inu anthu a ku Giliyadi mukukhala mʼdera la Efuraimu ndi la Manase, ndinu anthu othawa ku Efuraimu.”