5 Amuna a ku Giliyadi anakatchinga powolokera Yorodano+ anthu a ku Efuraimu asanafike. Ndiyeno munthu aliyense wa ku Efuraimu amene ankathawa akanena kuti: “Ndiloleni ndiwoloke,” amuna a ku Giliyadi ankamufunsa kuti: “Kodi ndiwe wa ku Efuraimu?” Akayankha kuti: “Ayi!”