16 Choncho mkazi wa Samisoni anayamba kulirira mwamuna wake, ndipo ankamuuza kuti: “Iwe umadana nane, sumandikonda.+ Wauza anthu a mtundu wanga mwambi, koma ine sunandiuze tanthauzo lake.” Atatero anamuuza kuti: “Ngakhale bambo kapena mayi anga sindinawauze. Ndiye iweyo ndikuuze chifukwa chiyani?”