18 Iye anayankha kuti: “Tikuchokera ku Betelehemu wa ku Yuda ndipo tikupita kudera lamapiri lakutali kwambiri la Efuraimu. Kumeneko ndiye kwathu. Ndinapita ku Betelehemu wa ku Yuda+ ndipo panopa ndikupita kunyumba ya Yehova, koma palibe amene wanditenga kuti ndikagone kunyumba kwake.