22 Abambo awo kapena azichimwene awo akabwera kudzadandaula, tidzawauza kuti, ‘Tikomereni mtima, tiyeni tiwathandize, chifukwa pa nthawi ya nkhondo, sitinakwanitse kugwira akazi okwanira amuna onse a fuko la Benjamini.+ Ndipo inunso simukanawapatsa akazi popanda kukhala ndi mlandu.’”+