13 Atafika, anapeza Eli atakhala pampando mʼmbali mwa msewu, maso ali kunjira, chifukwa ankachita mantha kwambiri akaganizira za Likasa la Mulungu woona.+ Munthuyo analowa mumzindawo kukanena za nkhondoyo, ndipo anthu onse amumzindawo anayamba kulira.