2 Sauli anasankha amuna 3,000 a mu Isiraeli. Pa amunawa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi komanso kudera lamapiri la Beteli. Pamene amuna 1,000 anali ndi Yonatani+ ku Gibeya+ wa ku Benjamini. Anthu ena onse otsalawo anawauza kuti abwerere kumatenti awo.