25 Kenako Sauli anafika ndi asilikali ake kudzafunafuna Davide.+ Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anakabisala kuthanthwe,+ ndipo anapitiriza kukhala mʼchipululu cha Maoni. Sauli atauzidwa zimenezi anayamba kusakasaka Davide mʼchipululu cha Maoni.