14 Nthawi yomweyo Sauli anafunsa mzimayiyo kuti: “Akuoneka bwanji?” Mzimayiyo anayankha kuti: “Akuoneka kuti ndi mwamuna wokalamba ndipo wavala mkanjo wodula manja.”+ Sauli atamva zimenezi, anazindikira kuti ndi “Samueli” ndipo Sauliyo anagwada nʼkumuweramira mpaka nkhope yake kufika pansi.