6 Choncho Akisi+ anaitana Davide nʼkumuuza kuti: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova, Mulungu wamoyo, iweyo ndiwe wolungama ndipo ndikanakonda kupita nawe kunkhondo,+ chifukwa sindinakupeze ndi vuto lililonse kuyambira tsiku limene unabwera kwa ine mpaka lero.+ Koma olamulira ena sakukukhulupirira.+