8 Mutu wa Isi-bosetiwo+ anafika nawo kwa Davide ku Heburoni ndipo anauza mfumuyo kuti: “Takubweretserani mutu wa Isi-boseti mwana wa mdani wanu Sauli,+ amene ankafunafuna moyo wanu.+ Lero Yehova wabwezera Sauli ndi mbadwa zake pa zimene anakuchitirani inu mbuyanga mfumu.”