20 Davide atabwerera kunyumba kwake kuti akadalitse banja lake, Mikala mwana wamkazi wa Sauli+ anatuluka kukakumana naye. Mikala anati: “Lero mfumu ya Isiraeli yaonetsa ulemerero wake podzivula pamaso pa akapolo aakazi a atumiki ake, ngati mmene munthu wopanda nzeru amadzivulira mopanda manyazi.”+