20 Davide atamva zimenezi, anadzuka pamene anagona paja ndipo anasamba nʼkudzola mafuta.+ Kenako anasintha zovala zake nʼkukalowa mʼnyumba+ ya Yehova kukalambira. Atachoka kumeneko anakalowa mʼnyumba yake nʼkupempha kuti amupatse chakudya ndipo anadya.