11 Koma mayiyo anati: “Chonde mfumu, kumbukirani Yehova Mulungu wanu kuti munthu wobwezera magazi+ asachite zoipa zina komanso asaphe mwana wanga.” Ndiyeno mfumu inati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo,+ ngakhale tsitsi limodzi la mwana wako siligwa pansi.”